December 28, 2020–January 3, 2021
LEVITIKO 16-17
Nyimbo 41 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Zimene Tingaphunzile pa Zocitika za pa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo”: (10 min.)
Lev. 16:12—Mophiphilitsa, mkulu wa ansembe anali kuonekela pamaso pa Yehova (w19.11 21 ¶4)
Lev. 16:13—Mkulu wa ansembe anali kufukiza zofukiza kwa Yehova (w19.11 21 ¶5)
Lev. 16:14, 15—Kenako mkulu wa ansembe anali kupeleka nsembe kuti aphimbe macimo a ansembe ndi a anthu (w19.11 21 ¶6)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Lev. 16:10—Kodi mbuzi ya Azazeli inacitila cithunzi nsembe ya Yesu m’njila ziti? (it-1 226 ¶3)
Lev. 17:10, 11—N’cifukwa ciani timakana kuikidwa magazi? (w14 11/15 10 ¶10)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Lev. 16:1-17 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso, loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 3)
Ulendo Wobwelelako: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Kenako gaŵilani buku lophunzitsila Baibo. (th phunzilo 4)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) fg phunzilo 1 ¶1-2 (th phunzilo 14)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kodi Mungakonde Kufunsila Kuti Mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu?”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Amishonale—Anchito Okolola.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) lfb phunzilo 12
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 35 na Pemphelo