UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Timaonetsa Cikondi Ngati Ticita Zinthu Mogwilizana na Cilango ca Yehova
Kucotsa mu mpingo anthu olakwa osalapa kumateteza mpingo, komanso ni cilango kwa anthu osalapawo. (1 Akor. 5:6, 11) Tikamacita zinthu mogwilizana na cilango ca Yehova cimeneci, timaonetsa kuti tili na cikondi. N’cifukwa ciani takamba conco pamene kucotsa munthu mu mpingo kumabweletsa cisoni kwa onse okhudzidwa, kuphatikizapo acibale apafupi komanso abale a m’komiti yaciweluzo?
Cacikulu kuposa zonse n’cakuti, ngati ticita zinthu mogwilizana na cilango ca Yehova, timaonetsa kuti timakonda dzina lake na miyezo yake yoyela. (1 Pet. 1:14-16) Timaonetsanso cikondi kwa wocotsedwayo. Zili conco cifukwa cilango camphamvu, olo cikhale cowawa, cingabale “cipatso camtendele comwe ndi cilungamo.” (Aheb. 12:5, 6, 11) Ngati tiyanjana na munthu wocotsedwa kapena wodzilekanitsa, timalepheletsa cilango ca Yehova kugwila nchito bwino. Kumbukilani kuti Yehova amalanga anthu ake “pa mlingo woyenela.” (Yer. 30:11) Timakhala na ciyembekezo cakuti munthu amene wacotsedwa adzabwelela kwa Atate wathu wacifundo. Koma palipano, timapitiliza kucita zinthu mogwilizana na cilango ca Yehova na kuyesetsa mmene tingathele kulimbitsa ubale wathu na Yehova.—Yes. 1:16-18; 55:7.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI KHALANIBE OKHULUPILIKA NA MTIMA WONSE, NDIPO PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
Kodi makolo acikhristu amamvela bwanji ngati mwana wawo wasiya Yehova?
-
Kodi mpingo ungawathandize bwanji acibale okhulupilika a munthu wocotsedwa?
-
Ni nkhani iti ya m’Baibo imene imaonetsa kufunika kokhala wokhulupilika kwambili kwa Yehova kuposa kwa acibale athu?
-
Timaonetsa bwanji kuti ndife okhulupilika kwambili kwa Yehova kuposa kwa acibale athu?