Alongo akugaŵila kabuku ka mutu wakuti Mvetselani kwa Mulungu ku Indonesia

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO February 2016

Maulaliki Acitsanzo

Mmene tingagaŵile Galamukani! ndiponso kabuku ka mutu wakuti Mvetselani kwa Mulungu. Lembani ulaliki wanu mwa kutengela maulaliki acitsanzo.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Nehemiya Anali Kukonda Kulambila Koona

Ganizilani khama limene Nehemiya anaonetsa pomanga mpanda wa Yerusalemu ndi kupititsa patsogolo kulambila koona. (Nehemiya 1-4)

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Nehemiya Anali Woyang’anila wa Citsanzo Cabwino Kwambili

Nehemiya anathandizila Aisiraeli kukhala osangalala polambila Mulungu. Ganizilani mmene zinthu zinalili ku Yerusalemu m’mwezi wa Tishiri mu 455 B.C.E. (Nehemiya 8:1-18)

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Olambila Okhulupilika Amacilikiza Dongosolo la Gulu la Mulungu

Anthu a Yehova m’nthawi ya Nehemiya anacilikiza kulambila koona m’njila zambili ndi mtima wonse. (Nehemiya 9-11)

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Umoyo Wabwino Koposa

Acinyamata amene ali m’gulu la Yehova, ali ndi mipata yambili yokhala ndi umoyo waphindu. Mafunso okambilana mfundo za m’vidiyo ya mutu wakuti Umoyo Wabwino Koposa.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Zimene Tikuphunzila m’Buku la Nehemiya

Ganizilani mmene Nehemiya anaonetsela cangu poteteza kulambila koona. (Nehemiya 12-13)

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Itanilani Anthu Ambili a m’Gawo Lanu ku Cikumbutso

Ulaliki wa citsanzo ca mmene tingagaŵile kapepala koitanila anthu ku Cikumbutso mu 2016. Tsatilani malangizo a mmene mungakulitsile cidwi ca mwini nyumba.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Esitere Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

Ganizilani mmene anaonetsela kulimba mtima poteteza anthu a Mulungu. (Esitere 1-5)