UMOYO WATHU WACIKRISTU
Umoyo Wabwino Koposa
Acinyamata amene ali m’gulu la Yehova, ali ndi mipata yambili yotumikila Yehova. Onelelani vidiyo ya mutu wakuti Umoyo Wabwino Koposa (The Best Life Ever) kuti muone mmene Cameron anagwilitsila nchito nthawi yake mwanzelu monga wacinyamata. Kenako yankhani mafunso otsatilawa. (Pitani pa jw.org, ndi kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > TEENAGERS.)
-
Ndi nchito iti imene Cameron amakonda kwambili kucita?
-
Ndi liti pamene anaganiza zoonjezela utumiki wake? Nanga anacita liti zimenezo?
-
N’ciani cinamuthandiza kukonzekela kukatumikila ku dela limene kuli ofalitsa ocepa m’dziko lina?
-
Ndi mavuto otani amene Cameron anakumana nao pamene anali kutumikila m’dziko lina?
-
N’cifukwa ciani n’zopindulitsa kutumikila Yehova ku dela lacilendo?
-
Ndi madalitso otani amene Cameron anakhala nao?
-
N’cifukwa ciani kutumikila Yehova ndiye umoyo wabwino koposa?
-
Ndi mipata ina iti imene acinyamata ali nayo m’gulu la Yehova?