February 29– March 6
ESITERE 1–5
Nyimbo 86 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Esitere Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu”: (Mph. 10)
[Onetsani Vidiyo Yofotokoza Buku la Esitere.]
Esitere 3:5-9—Hamani anafuna kupha anthu onse a Mulungu (ia tsa. 131 ndime 18-19)
Esitere 4:11–5:2—Esitere anali ndi cikhulupililo colimba cakuti sanaope kufa (ia tsa. 125 ndime 2; tsa. 134 ndime 24-26)
Kufufuza Cuma Cakuuzimu: (Mph. 8)
Esitere 2:15—Kodi Estere anaonetsa bwanji kuti anali wodzicepetsa ndi wodziletsa? (w06 CN 3/1 tsa. 9 ndime 8)
Esitere 3:2-4—N’cifukwa ciani Moredekai anali kukana kugwadila Hamani? (ia tsa. 131 ndime 18)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kundiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: Esitere 1:1-15 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Gaŵilani kabuku ka mutu wakuti Mvetselani kwa Mulungu. Ndiyeno yalani maziko a ulendo wobwelelako
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa wofalitsa akucita ulendo wobwelelako kwa munthu amene analandila kabuku ka mutu wakuti Mvetselani kwa Mulungu. Kambilanani tsamba 2 ndi 3 ndi kuyala maziko a ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene mungacititsile phunzilo la Baibulo mwa kugwilitsila nchito kabuku ka mutu wakuti, Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya, tsamba 4 ndi 5 kwa mwininyumba amene analandila kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu pa ulendo woyamba. (km 7/12 tsa. 2-3 ndime 4)
UMOYO WATHU WACIKRISTU
Zosoŵa za pampingo: (Mph. 10)
Kodi Mukupindula Bwanji ndi Makonzedwe Atsopano a Msonkhano komanso Kabuku ka Msonkhano?: (Mph. 5) Nkhani yokambilana. Pemphani omvela kufotokoza mmene apindulila ndi makonzedwe atsopano a msonkhano wa mkati mwa mlungu. Limbikitsani onse kuti azikonzekela bwino msonkhanowu kuti azipindula kwambili.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia mutu 10 ndime 1-11, ndi bokosi pa tsa. 86 (Mph. 30)
Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi Kufotokoza Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wamaŵa. (Mph. 3)
Nyimbo 113 ndi Pemphelo