Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | ESITERE 1–5

Esitere Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

Esitere Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

Esitere anaonetsa cikhulupililo camphamvu ndiponso kulimba mtima poteteza anthu a Mulungu

  • Aliyense wopita kukaonekela kwa Mfumu osaitanidwa anali kuphedwa. Panali patapita masiku 30 Esitere asanaitanidwe kukaonekela kwa mfumu

  • Mfumu Ahasiwero amene anthu ambili amakhulupilila kuti anali Sasita woyamba, anali ndi mtima wapacala kwambili. Panthawi ina, iye analamula kuti munthu wina adulidwe pakati, ndipo mtembo wake uikidwe poonekela kuti anthu ena atengelepo phunzilo. Ahasiwero anacotsanso Vasiti paufumukazi cifukwa cakuti anakana kumvela zonena zake

  • Esitere anafunika kuulula kuti anali Myuda ndi kuthandiza mfumu kutsimikizila kuti mlangizi wake amene anali kum’khulupilila kwambili anali atam’namiza