February 8- 14
NEHEMIYA 5-8
Nyimbo 123 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Nehemiya anali woyang’anila wa citsanzo cabwino kwambili”: (Mph. 10)
Neh. 5:1-7—Nehemiya anamvela zimene anthu anali kukamba, ndipo anacitapo kanthu (w06 2/1 tsa. 9 ndime 2)
Neh. 5:14-19—Nehemiya anaonetsa kudzicepetsa, kusadzikonda, ndi kuzindikila (w06 2/1 tsa. 10 ndime 4)
Neh. 8:8-12—Nehemiya anagwila nao nchito yopeleka malangizo akuuzimu kwa anthu (w06 2/1 tsa. 11 ndime 4)
Kufufuza Cuma Cakuuzimu: (Mph. 8.)
Neh. 6:5—N’cifukwa ciani Sanibalati anatumiza “kalata yosatseka” kwa Nehemiya? (w06 2/1 tsa.9 ndime 3)
Ne 6:10-13—N’cifukwa ciani Nehemiya sanavomeleze malangizo a Semaya? (w07 7/1 tsa 30 ndime 15)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kundiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: Neh. 6:14–7:7a (Mph. 4 kapena zocepelepo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Gaŵilani magazini ya Galamukani! pogwilitsila nchito nkhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto. Ndiyeno yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa wofalitsa akucita ulendo wobwelelako kwa munthu amene anaonetsa cidwi pankhani zofotokoza mutu wa pacikuto ca Galamukani! imene munamugaŵila. Ndiyeno yalani maziko a ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene mungacititsile phunzilo la Baibulo (bh tsa. 28-29 ndime 4-5)
UMOYO WATHU WACIKRISTU
Kodi Mukukalamila Udindo?: (Mph. 15) Nkhani yokambidwa ndi mkulu yocokela mu Nsanja ya Mlonda ya September 15, 2014, tsamba 3-6. Onetsani vidiyo ya mutu wakuti Abale, Kalamilani Nchito Yabwino, imene inaonetsedwa mu December 2015 pa TV ya Mboni za Yehova ya JW Broadcasting. Gogomezelani zifukwa zoyenelela zokalamilila maudindo, ndi mmene m’bale angacitile zimenezo. Limbikitsani abale onse mokoma mtima kuti ayenela kukalamila kukhala atumiki othandiza kapena akulu.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia Mutu 8 ndime 17-27, kubwelelamo pa tsa. 75 (Mph. 30)
Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi Kufotokoza Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wamaŵa (Mph. 3)
Nyimbo 125 ndi Pemphelo