Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Itanilani Anthu Ambili a m’Gawo Lanu ku Cikumbutso

Itanilani Anthu Ambili a m’Gawo Lanu ku Cikumbutso

Nchito yapadela yoitanila anthu ku Cikumbutso idzayamba pa February 27. Panthawiyo, tiyenela kuitanila anthu ambili a m’gawo lathu kuti adzacite nafe Cikumbutso ca imfa ya Kristu. Tiyenelanso kupeleka cisamalilo cacikulu kwa anthu amene angaonetse cidwi n’colinga cakuti tikulitse cidwico.

ZIMENE MUYENELA KUCITA

KAMBANI ULALIKI WANU

“Tikugaŵila kapepala kokuitanilani ku mwambo wofunika kwambili. Pa March 23, anthu mamiliyoni ambili pa dziko lonse lapansi adzabwela ku mwambo wokumbukila imfa ya Yesu Kristu ndi kumvetsela nkhani ya m’Baibulo imene idzafotokoza mmene timapindulila ndi imfa yake. Kapepalaka kaonetsa nthawi ndi malo kumene tidzacitila mwambowu kuno kwathu. Tikupemphani kuti mudzapezekepo.”

Ngati mwininyumba waonetsa cidwi . . .

  • GAŴILANI NSANJA YA MLONDA

    Yalani maziko a ulendo wobwelelako.

  • ONETSANI VIDIYO YA CIKUMBUTSO

    Yalani maziko a ulendo wobwelelako.

Pa ulendo wobwelelako,  . . .

  • MUONETSENI KAVIDIYO KA MUTU WAKUTI N’CIFUKWA CIANI MUYENELA KUPHUNZILA BAIBULO?

    Kenako gaŵilani cofalitsa cothandiza kuphunzila Baibulo.

  • GAŴILANI BUKU LA MUTU WAKUTI ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA M’CENI-CENI

    Fotokozani mfundo zoonjezeleka zokhudza Cikumbutsa zopezeka patsamba 206-208. Kenako gaŵilani bukulo.

  • GAŴILANI KABUKU KA MUTU WAKUTI MVETSELANI KWA MULUNGU

    Kambilanani tanthauzo la imfa ya Kristu mwa kugwilitsila nchito mfundo zili patsamba 18-19. Kenako gaŵilani kabukuko.