UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO February 2017
Maulaliki a Citsanzo
Maulaliki a citsanzo oseŵenzetsa pogaŵila Galamukani! ndi mfundo ya coonadi ca m’Baibo yokhudza tsogolo labwino. Seŵenzetsani maulaliki a citsanzo pokonza ulaliki wanu.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Kumvela Yehova Kumabweletsa Madalitso
Mwacikondi Yehova amationetsa njila imene tiyenela kuyendamo.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Khristu Anavutika Cifukwa ca Ife
Imfa ya Yesu inapeleka yankho pa zimene Satana anakamba zokhudza kukhulupilika kwa atumiki a Mulungu
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo Colimba mwa Mlengi Wawo
Kodi ana anu amakhulupilila ciani pankhani yokhudza mmene moyo unayambila? Kodi mungawathandize bwanji kukhala na cikhulupililo cakuti Yehova Mulungu ndiye Mlengi?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Ndikalengeze za Caka ca Yehova Cokomela Anthu Mtima”
Kodi caka ca Yehova cokomela anthu mtima ni caka ceni-ceni? Kodi nthawi imeneyi igwilizana bwanji na nchito yolalikila?
UMOYO WACIKHRISTU
Muzigaŵila Zofalitsa Mwanzelu
Kuti zofalitsa zathu zipulintidwe ndi kutumizidwa ku mipingo padziko lonse, pamacitika nchito yaikulu komanso pamawonongeka ndalama zambili. Tizisamala pogaŵila zofalitsa kwa anthu.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano Zidzabweletsa Cisangalalo Cacikulu
Kodi lonjezo la Mulungu la “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano” litanthauzanji kwa ise masiku ano?
UMOYO WACIKHRISTU
Kondwelani mu Ciyembekezo Canu
Ciyembekezo cili ngati nangula. Kusinkha-sinkha malonjezo a m’Mau a Mulungu kumatithandiza kukhalabe okondwela ndi okhulupilika tikayang’anizana ndi mavuto amene ali ngati cimphepo ca mkuntho panyanja.