February 13- 19
YESAYA 52-57
Nyimbo 148 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Khristu Anavutika Cifukwa ca Ife”: (10 min.)
Yes. 53:3-5—Iye ananyozewa, na kuphwanyiwa cifukwa ca zocimwa zathu (w09 1/15 peji 26 pala. 3-5)
Yes. 53:7, 8—Na mtima wonse, Khristu anapeleka moyo wake cifukwa ca ise (w09 1/15 peji 27 pala. 10)
Yes. 53:11, 12—Tikhoza kukhala olungama cifukwa iye anakhalabe wokhulupilika mpaka imfa (w09 1/15 peji 28 pala. 13)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yes. 54:1—Kodi “mkazi wosabeleka” wochulidwa mu ulosi umenewu n’ndani? Nanga “ana” ake n’ndani? (w06 3/15 peji 11 pala. 2)
Yes. 57:15—Kodi Yehova “amakhala” na munthu “wopsinjika” ndi “wa mtima wodzicepetsa” m’lingalilo lanji? (w05 10/15 peji 26 pala. 3)
Kodi ine pacanga, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino zimene ine pacanga ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yes. 57:1-11
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) Gaŵilani kabuku ka Mvetselani kwa Mulungu, nakuyala maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) Citani citsanzo coonetsa ulendo wobwelelako kwa munthu amene analandila kabuku ka Mvetselani. Kambilanani mapeji 2-3, ndiyeno yalani maziko a ulendo wina wobwelelako.
Phunzilo la Baibo: (6 mineti kapena kucepelapo) bh peji 14-15 pala. 16-17—Ngati n’zotheka, tate acititse phunzilo kwa mwana wake mwamuna kapena mkazi.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo Colimba mwa Mlengi Wawo”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani Vidiyo yakuti Zimene Acicepele Anzanu Amakamba—Kukhulupilila mwa Mulungu. (yendani ku mavidiyo pa ACICEPELE).
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 8 pala. 8-13, na chati pa peji 83”
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 107 na Pemphelo