YESAYA 52-57
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU |Khristu Anavutika Cifukwa ca Ife
“Ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa . . . Tinamuona ngati wosautsidwa wokwapulidwa ndi Mulungu ndiponso wozunzidwa”
53:3-5
-
Anthu anam’nyoza Yesu na kum’namizila kuti anali kunyoza Mulungu. Ena anaganiza kuti Mulungu anali kum’langa
“Koma zinamukomela Yehova kuti mtumiki wake aphwanyidwe. . . . Ndipo ndi dzanja lake, adzakwanilitsa zokonda Yehova”
53:10
-
Sitikukaika kuti cinamuŵaŵa kwambili Yehova kuona Mwana wake akuphedwa. Ngakhale n’conco, iye anakondwela kwambili na kukhulupilika kwa Yesu. Imfa ya Yesu inapeleka yankho pa zimene Satana anakamba zokhudza kukhulupilika kwa atumiki a Mulungu. Ndipo inabweletsa madalitso kwa anthu olapa. Conco, inathandiza kuti “cifunilo ca Mulungu” cikwanilitsike.