UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo Colimba mwa Mlengi Wawo
Cilengedwe cimalengeza ulemelelo wa Yehova. (Sal. 19:1-4; 139:14) Koma dziko la Mdyelekezi limalimbikitsa ziphunzitso zotsutsa mfundo yakuti Mulungu ndiye anapanga moyo. (Aroma 1:18-25) Kodi mungateteze bwanji ana anu ku ziphunzitso zimenezo kuti zisazike mizu m’maganizo na m’mitima yawo? Ayambilileni ali aang’ono. Athandizeni kukhulupilila kuti Yehova aliko, ndipo amasamala za iwo aliyense payekha-payekha. (2 Akor. 10:4, 5; Aef. 6:16) Yesani kudziŵa zimene iwo amaganiza pa zinthu zimene amaphunzila ku Sukulu. Ndiyeno seŵenzetsani zida zambili zimene tili nazo kuti muwafike pamtima.—Miy. 20:5; Yak. 1:19.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE ACICEPELE ANZANU AMAKAMBA—KUKHULUPILILA MWA MULUNGU, NDIYENO KAMBILANANI MAFUNSO AYA:
Kodi ambili amati ciani pa nkhani yokhulupilila Mulungu?
Nanga kusukulu kwanu amaphunzitsa ciani pa nkhani imeneyi?
N’ciani cimakukhutilitsani kuti Yehova aliko?
Mungam’thandize bwanji munthu wina kukhulupilila kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse?