Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 58-62

“Ndikalengeze za Caka ca Yehova Cokomela Anthu Mtima”

“Ndikalengeze za Caka ca Yehova Cokomela Anthu Mtima”

“Caka ca Yehova cokomela anthu mtima” si caka ceni-ceni

61:1, 2

  • Ni nthawi imene Yehova amapatsa anthu ofatsa mpata wolabadila ufulu umene iye akulengeza

  • M’zaka 100 zoyambilila, caka cokomela anthu mtima cinayamba pamene Yesu anayamba utumiki wake mu 29 C.E, ndipo cinatha pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E., “pa tsiku lobwezela” la Yehova.

  • M’nthawi yathu ino, caka cokomela anthu mtima cinayamba pamene Yesu analongedwa ufumu mu 1914, ndipo cidzatha pa cisautso cacikulu

Yehova adalitsa anthu ake ndi “mitengo ikulu-ikulu ya cilungamo”

61:3, 4

  • Kaŵili-kaŵili mitengo itali-itali imakulila pamodzi m’nkhalango, ndipo mtengo uliwonse umacilikiza unzake

  • Mizu ya mitengo imapotana-potana, kumanganitsa mitengoyo pansi, cakuti siingagwe na cimphepo camkuntho

  • Mitengo itali-italiyo imapeleka mthunzi ku tumitengo tung’ono-tung’ono na zomela zina, ndipo masamba amene amagwa amacititsa nthaka kukhala yaconde

Abale na alongo onse mumpingo wacikhristu padziko lonse, amapindula ndi citetezo na cicilikizo ca “mitengo ikulu-ikulu ya cilungamo,” imene ni otsalila odzozedwa