Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WACIKHRISTU

Kondwelani mu Ciyembekezo Canu

Kondwelani mu Ciyembekezo Canu

Ciyembekezo cili ngati nangula. (Aheb. 6:19) Cimatithandiza kuti cikhulupililo cathu cisawonongeke, ngati mmene ngalawa imawonongekela ndi cimphepo ca mkuntho panyanja. (1 Tim. 1:18, 19) Mphepo zamkuntho zingaphatikizepo kugwilitsidwa mwala, kutaikidwa cuma, matenda amgonagona [osacila msanga], imfa ya wokondedwa, kapena vuto lililonse loopseza cikhulupililo cathu.

Cikhulupililo na ciyembekezo zimatithandidza kuona bwino mphoto yathu yamtsogolo. (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 11:13, 26, 27) Conco, kaya ciyembekezo cathu n’ca kumwamba kapena padziko lapansi, tiyenela kucilimilila nthawi zonse mwa kusinkha-sinkha malonjezo ali m’Mau a Mulungu. Ndiyeno pamene mayeselo ativutitsa maganizo, tidzakhalabe acimwemwe.—1 Pet. 1:6, 7.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI KONDWELANI NDI CIYEMBEKEZO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • N’cifukwa ciani Mose n’citsanzo cabwino cofunika kutengela?

  • Mitu ya mabanja ili na udindo wanji?

  • Ni nkhani ziti zimene mungakambilane pa Kulambila kwa Pabanja lanu?

  • Kodi ciyembekezo cingakuthandizeni bwanji kuyang’anizana ndi mayeselo mwacidalilo?

  • N’ciani cimene imwe muyembekezela mwacidwi m’tsogolo?