Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 63-66

Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano Zidzabweletsa Cisangalalo Cacikulu

Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano Zidzabweletsa Cisangalalo Cacikulu

Lonjezo la Mulungu lokonzanso zinthu la m’caputa 65 ca Yesaya, ni lotsimikizika cakuti Yehova akamba monga kuti linakwanilitsika kale.

Yehova alenga kumwamba kwatsopano na dziko lapansi latsopano mmene zinthu zakale sizidzakumbukikanso

65:17

Kodi kumwamba kwatsopano n’ciani?

  • Ni boma latsopano limene lidzakonza zinthu padziko lapansi

  • Linakhazikitsidwa mu 1914 pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu

Nanga dziko lapansi latsopano n’ciani?

  • Ni citaganya ca anthu a m’maiko onse, zinenelo, na mafuko osiyana-siyana. Ndipo iwo amagonjela ulamulilo wa boma latsopano lakumwamba

Kodi zinthu zakale sizidzakumbukika motani?

  • Kudzakhala kulibe mavuto, matenda, kapena zovutitsa maganizo zilizonse.

  • Anthu okhulupilika adzakondwela kwambili ndi umoyo ndipo azidzayamikila akaganizila zinthu zabwino zimene anacita tsiku lapita