February 6- 12
YESAYA 47-51
Nyimbo 120 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Kumvela Yehova Kumabweletsa Madalitso”: (10 min.)
Yes. 48:17—Kulambila koona n’kozikidwa pa kumvela malangizo a Mulungu (ip-2 131 pala. 18)
Yes. 48:18—Yehova amatikonda ndipo amafuna kuti tizikondwela na umoyo (ip-2 peji 131 pala. 19)
Yes. 48:19—Kumvela kumabweletsa madalitso osatha (ip-2 peji 132 pala. 20-21)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yes. 49:6—Kodi Mesiya anakhala bwanji “kuwala kwa mitundu ya anthu,” ngakhale kuti utumiki wake padziko lapansi unalekezela kwa Aisiraeli okha? (w07 1/15 peji 9 pala. 8)
Yes. 50:1—N’cifukwa ninji Yehova anafunsa Aisiraeli kuti: “Cili kuti cikalata cothetsela ukwati wa mayi wanu yemwe ndinamuthamangitsa?” (it-1 peji 643 pala. 4-5)
Kodi ine pacanga, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino zimene ine pacanga ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yes. 51:12-23
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (15 min.) Kukambilana kozikidwa pa “Maulaliki a Citsanzo.” Tambitsani vidiyo yake iliyonse, kenako kambilanani zimene mwaphunzilapo.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zosoŵa za Pampingo: (7 min.) Mungasankhe kukambilana zimene tiphunzilapo m’nkhani yopezeka mu Buku Lapacaka la 2016 pa mapeji 144-145)
Khala Bwenzi la Yehova—Mvela Yehova: (8 min.) Kukambilana. Yambani mwa kutambitsa vidiyo yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Mvela Yehova (Yendani ku mavidiyo pa ANA). Pambuyo pake, kambilanani mafunso aya: Kodi cifukwa cacikulu comvelela Yehova n’ciani? (Miy. 27:11) Ni njila zina ziti zimene ana angaonetsele kuti ni omvela kwa Yehova? Ni njila zina ziti zimene acikulile angaonetsele kuti ni omvela kwa Yehova?)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 8 pala. 1-7, na bokosi papeji 79.
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 98 na Pemphelo