Aphunzitsa coonadi ku Cambodia

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO February 2018

Makambilano a Citsanzo

Makambilano ozikidwa pa mafunso akuti: Kodi Baibo ikali yothandiza masiku ano? Kodi Baibo imagwilizana na sayansi? Kodi malangizo a m’Baibo ni othandiza?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Fanizo la Tiligu ndi Namsongole

Kodi Yesu akukamba za ciani m’fanizo ili? Kodi wofesa, mdani, na okolola akuimila ndani?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Mafanizo a Ufumu na Tanthauzo Lake Kwa Ise

Yesu anaseŵenzetsa mafanizo osavuta kumva pophunzitsa mfundo zozama za coonadi. Ni mfundo zina ziti zimene tingaphunzile mu Mateyu caputa 13?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Kudyetsa Anthu Ambili Mwa Kugwilitsila Nchito Anthu Ocepa

Yesu anauza ophunzila ake kuti adyetse khamu la anthu, ngakhale kuti anali cabe na mitanda isanu ya mkate na nsomba ziŵili. N’ciani cinacitika, nanga zitiphunzitsa ciani?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Uzilemekeza Atate Ako ndi Amayi Ako

Yesu anagogomeza lamulo lakuti uzilemekeza atate ako ndi amayi ako. Kodi lamulo ili lili na malile?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Kodi Muli na Maganizo a Ndani?

Kodi tifunika kucita ciani kuti tikwanilitse cifunilo ca Mulungu? Yesu anakamba zinthu zitatu zimene zingatithandize kupewa maganizo olakwika.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mafunso Mwaluso

Yesu anali kuwafunsa mafunso omvela ake powaphunzitsa mfundo zosiyana-siyana. Tingatengele bwanji luso lake la kaphunzitsidwe mu ulaliki?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Muzisamala Kuti Musadzipunthwitse Kapena Kupunthwitsa Ena

Yesu anaseŵenzetsa mafanizo pofuna kuphunzitsa za kuopsa kwa kudzipunthwitsa kapena kupunthwitsa ena. N’ciani cingakhale copunthwitsa mu umoyo wanu?