Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 14-15

Kudyetsa Anthu Ambili Mwa Kugwilitsila Nchito Anthu Ocepa

Kudyetsa Anthu Ambili Mwa Kugwilitsila Nchito Anthu Ocepa

Pasika wa mu 32 C.E. ali pafupi kucitika, Yesu anacita cozizwitsa cimene olemba Mauthenga Abwino onse anayi anacilemba.

Mwa cozizwitsa cimeneco, Yesu anakhazikitsa njila kapena kuti chanelo imene akuigwilitsilabe nchito masiku ano.

14:16-21

  • Yesu anauza ophunzila ake kuti adyetse khamu la anthu, ngakhale kuti anali cabe na mitanda isanu ya mkate na nsomba ziŵili

  • Yesu atatenga mitanda ya mkate na nsomba zija, anapemphela. Kenako, anagaŵila ophunzila ake, amenenso anagaŵila khamu la anthu

  • Mozizwitsa, panakhala cakudya cokwanila aliyense kudya na kutsalako. Yesu anadyetsa anthu masauzande mwa kugwilitsila nchito anthu ocepa—ophunzila ake

  • Yesu anakambilatu kuti m’masiku otsiliza, adzakhazikitsa njila kapena kuti chanelo yopelekela cakudya cauzimu “pa nthawi yoyenela.”—Mat. 24:45

  • Mu 1919, Yesu anasankha “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” kagulu kocepa ka abale odzozedwa, kuti aziyang’anila “anchito ake apakhomo,” amene amapatsidwa cakudya ca kuuzimu

  • Kupitila m’kagulu kocepa kameneka ka abale odzozedwa, Yesu akutsatila njila imene anakhazikitsa m’nthawi ya atumwi

Ningaonetse bwanji kuti nimalemekeza njila kapena kuti chanelo imene Yesu amaiseŵenzetsa popatsa anthu cakudya ca kuuzimu?