Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Uzilemekeza Atate Ako ndi Amayi Ako

Uzilemekeza Atate Ako ndi Amayi Ako

Yesu ali pa dziko lapansi, anagogomeza lamulo lakuti: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (Eks. 20:12; Mat. 15:4) Yesu anali na ufulu wolankhula cifukwa ali wacicepele, anali kumvela makolo ake. (Luka 2:51) Atakula, anaonetsetsa kuti amayi ake adzasamalilidwa bwino iye akamwalila.—Yoh. 19:26, 27.

Masiku anonso, Akhristu acicepele amene amamvela makolo awo, na kukamba nawo mwaulemu, amaonetsa kuti amawalemekeza. Lamulo lolemekeza makolo athu lilibe malile. Ngakhale makolo athu akalambe, tifunika kupitiliza kuwalemekeza mwa kumvela malangizo awo anzelu. (Miy. 23:22) Timaonetsanso kuti timalemekeza makolo athu okalamba mwa kuwathandiza akavutika maganizo komanso kuwasamalila mwa kuthupi ngati pafunika kutelo. (1 Tim. 5:8) Kaya ndise acicepele kapena acikulile, kukambilana bwino na makolo athu ndiyo njila yabwino yoonetsela kuti timawalemekeza.

TAMBANI VIDIYO YA TUKADOLI YAKUTI NINGAKAMBE NAWO BWANJI MAKOLO ANGA? NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • N’ciani cingacititse kuti zikhale zovuta kukamba na makolo anu?

  • Kodi mungawaonetse bwanji ulemu makolo anu pokamba nawo?

  • N’cifukwa ciani simuyenela kuleka kukamba na makolo anu? (Miy. 15:22)

    Kukambilana na makolo anu kungakuthandizeni kukhala na umoyo wopambana