Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mafunso Mwaluso

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mafunso Mwaluso

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Ngati “maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya,” ndiye kuti mafunso ali ngati cikopo cowatapila. (Miy. 20:5) Mafunso amacititsa omvela kukambapo maganizo awo. Mayankho a mafunso okonzewa bwino, nthawi zambili amatithandiza kudziŵa maganizo a munthu. Yesu anaseŵenzetsa mafunso mwaluso. Tingatengele bwanji citsanzo cake?

MMENE TINGACITILE:

  • Muzifunsa mafunso akuti muganiza bwanji. Yesu anafunsa ophunzila ake mafunso otsatizana kuti adziŵe maganizo awo. (Mat. 16:13-16; be peji 238 mapa. 3-5) Ni mafunso ati amene mungafunse womvela kuti akambe maganizo ake?

  • Muzifunsa mafunso othandizila. Yesu pofuna kuwongolela maganizo a Petulo, anafunsa mafunso na kupeleka mayankho othekela kuti Petulo aganizile yankho lolondola. (Mat. 17:24-26) Ni mafunso ati othandizila amene mungafunse kuti munthu apeze yankho lolondola?

  • Muzimuyamikila womvela wanu. Pamene mlembi ‘anayankha mwanzelu,’ Yesu anamuyamikila. (Maliko 12:34) Kodi imwe mungati ciani kwa munthu amene wayankha bwino funso?

TAMBANI MBALI YOYAMBA YA VIDIYO YAKUTI GWILANI NCHITO IMENE YESU ANAGWILA—PHUNZITSANI, NDIYENO, YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • N’cifukwa ciani citsanzo ici ca kaphunzitsidwe si cabwino olo kuti uthenga unali wolondola?

  • N’cifukwa ciani sitifunika kufotokoza uthenga cabe?

TAMBANI MBALI YACIŴILI YA VIDIYOYI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi m’bale anali kufunsa bwanji mafunso mwaluso?

  • Ni mbali zina ziti za kaphunzitsidwe kake zimene tingatengeleko?

Kodi kaphunzitsidwe kathu kangawakhudze bwanji anthu ena? (Luka 24:32)