Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 18-19

Muzisamala Kuti Musadzipunthwitse Kapena Kupunthwitsa Ena

Muzisamala Kuti Musadzipunthwitse Kapena Kupunthwitsa Ena

Yesu anaseŵenzetsa mafanizo pofuna kuphunzitsa za kuopsa kwa kudzipunthwitsa kapena kupunthwitsa ena.

18:6, 7

  • Liu lakuti “copunthwitsa” limatanthauza zocita kapena mikhalidwe imene ingacititse munthu kutsatila njila yolakwika, kupunthwa kapena kugwa m’makhalidwe, kapena kugwela m’chimo.

  • Munthu amene amapunthwitsa ena cingakhale bwino kumuponya m’nyanja atamangililidwa cimwala ca mphelo m’khosi mwake

Miyala ya Mphelo

18:8, 9

  • Yesu analangiza otsatila ake kuti ayenela kucotsa ngakhale cinthu cofunika ngako monga dzanja kapena diso ngati cimawapangitsa kupunthwa

  • Cingakhale bwino kucotsa ciwaloco kuti tikaloŵe mu Ufumu wa Mulungu kuposa kucisunga ndi kupita ku Gehena, kutanthauza ciwonongeko cothelatu

Mu umoyo wanga, n’ciani cingakhale copunthwitsa? Nanga ningapewe bwanji kudzipunthwitsa kapena kupunthwitsa ena?