February 5-11
MATEYU 12-13
Nyimbo 27 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Fanizo la Tiligu ndi Namsongole”: (10 min.)
Mat. 13:24-26—Munthu wina anafesa mbewu zabwino m’munda mwake, ndiyeno mdani wake anafesa namsongole m’mundamo (w13 7/1 mape. 15-16 mapa. 2-3)
Mat. 13:27-29—Tiligu ndi namsongole zinakulila pamodzi mpaka nthawi yokolola (w13 7/1 peji 16 pala. 4)
Mat. 13:30—Pa nthawi yokolola, coyamba okolola anasonkhanitsa namsongole pamodzi, kenako anasonkhanitsa tiligu (w13 7/1 mape. 18-19 mapa. 10-12)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Mat. 12:20—Kodi tingatengele bwanji cifundo ca Yesu? (nwtsty mfundo younikila)
Mat. 13:25—Kodi n’zoona kuti kale anthu anali kufesa namsongole m’minda ya anthu ena? (w16.10 peji 32)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Mat. 12:1-21
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyo.
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (3 min. olo kucepelelapo) Seŵenzetsani makambilano a citsanzo.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) bhs mape. 22-23 mapa. 10-12
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zofunikila za Mpingo: (5 min.)
“Mafanizo a Ufumu na Tanthauzo Lake Kwa Ise”: (10 min) Kambilanani mmene mafanizo amenewa amakhudzila utumiki wathu.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy Mutu 7
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 10 na Pemphelo