Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 12-13

Fanizo la Tiligu ndi Namsongole

Fanizo la Tiligu ndi Namsongole

Yesu anaseŵenzetsa fanizo la tiligu ndi namsongole pofuna kuonetsa mmene adzatengela gulu lonse la Akhristu odzozedwa pakati pa anthu, ndi kuti Akhristuwo adzayamba kudzozedwa kuyambila mu 33 C.E.

13:24

‘Munthu anafesa mbewu zabwino m’munda mwake’

  • Wofesa: Yesu Khristu

  • Mbewu zabwino zifesedwa: Ophunzila a Yesu adzozedwa na mzimu woyela

  • Munda: Anthu onse pa dziko lapansi

13:25

“Anthu ali m’tulo, kunabwela mdani wake. Mdaniyo anafesa namsongole”

  • Mdani: Mdyelekezi

  • Anthu ali m’tulo: Imfa ya atumwi

13:30

“Zilekeni zonse zikulile pamodzi mpaka nthawi yokolola”

  • Tiligu: Akhristu odzozedwa

  • Namsongole: Akhristu onama

“Coyamba sonkhanitsani namsongole . . . ; Mukatha mupite kukasonkhanitsa tiligu”

  • Akapolo/okolola: Angelo

  • Kusonkhanitsidwa kwa Namsongole: Kucotsewa kwa Akhristu onama pakati pa Akhristu odzozedwa

  • Kusonkhanitsila m’nkhokwe: Akhristu odzozedwa asonkhanitsidwa mumpingo umene unakhazikitsidwanso

Pamene nyengo yokolola inayamba, n’ciani cinasiyanitsa Akhristu oona na Akhristu onama?

Kodi kumvetsetsa fanizo ili kunganipindulitse bwanji ine panekha?