Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 4-6

“Mulungu Akuonetsa Cikondi Cake Kwa Ife”

“Mulungu Akuonetsa Cikondi Cake Kwa Ife”

5:8, 18, 21

Mphatso ya dipo imene Yehova anapeleka, ndiyo maziko othetsela nkhani zikulu-zikulu zokhudza cilengedwe conse, monga ya kuyeletsa dzina lake na kukweza ucifumu wake. Komanso, dipo limathandiza kuti Yehova azitiona kukhala olungama. Linapangitsanso kuti anthu onse omvela akhale na ciyembekezo ca tsogolo labwino.

Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso ya dipo?

  • Kudzipatulila na kubatizika kumaonetsa kuti timakhulupilila nsembe ya dipo, na kuti tifuna kukhala ku mbali ya Yehova

  • Kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumaonetsa kuti tikutengela citsanzo ca Yehova cokonda anthu amitundu yonse.—Mat. 22:39; Yoh. 3:16

Ni m’njila zinanso ziti zimene ningaonetsele ciyamikilo canga kwa Yehova pa mphatso ya dipo?