Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pitilizani Kuyembekezela Mopilila

Pitilizani Kuyembekezela Mopilila

Kodi Ufumu wa Mulungu mwauyembekezela kwa nthawi yaitali bwanji? Kodi mumapilila moleza mtima olo kuti mumakumana na mavuto? (Aroma 8:25) Akhristu ena amazondedwa, kuzunzidwa, kuikidwa m’ndende, ngakhale kuphedwa kumene. Ndipo ena ambili amapilila matenda osacilitsika kapena ukalamba.

N’ciani cingatithandize kuyembekezela mwacidwi olo tikumane na mavuto? Tifunika kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa kuŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha. Tifunikanso kusumika maganizo athu pa ciyembekezo. (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 12:2) Tifunika kupemphela mopembedzela kwa Yehova, na kum’pempha kuti atipatse mphamvu ya mzimu woyela. (Luka 11:10, 13; Aheb. 5:7) Atate wathu wacikondi adzatithandiza ‘kuti tithe kupilila zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso acimwemwe.’—Akol. 1:11.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI TIFUNIKA ‘KUTHAMANGA MOPILILA’—KHALANI NA CIDALILO CAKUTI MUDZALANDILA MPHOTO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Ni “zinthu zosayembekezeleka” ziti zimene zingatigwele mu umoyo? (Mlal. 9:11)

  • Kodi pemphelo lingatithandize bwanji tikakumana na mayeselo?

  • Ngati sitikwanitsa kucita zimene kale tinali kucita mu utumiki wa Yehova, n’cifukwa ciani tifunika kulunjika maganizo athu pa zimene tingakwanitse?

  • Yang’ananibe pa mphoto

    N’ciani cimakuthandizani kukhalabe na cidalilo cakuti mudzalandila mphoto?