February 25–March 3
AROMA 9-11
Nyimbo 25 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Fanizo la Mtengo wa Maolivi”: (10 min.)
Aroma 11:16—Mtengo wobzalidwa wa maolivi umaimila kukwanilitsidwa kwa colinga ca Mulungu cokhudza cipangano ca Abulahamu (w11 5/15 peji 23 pala. 13)
Aroma 11:17, 20, 21—Odzozedwa amene analumikizidwa ku mtengo wophiphilitsa wa maolivi ayenela kupitiliza kukhala na cikhulupililo (w11 5/15 peji 24 pala. 15)
Aroma 11:25, 26—Aisiraeli onse auzimu “adzapulumuka” (w11 5/15 peji 25 pala. 19)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Aroma 9:21-23—N’cifukwa ciani tiyenela kulola Yehova, Woumba Wamkulu kutiumba? (w13 7/1 peji 25 pala. 5)
Aroma 10:2—Tidziŵa bwanji kuti kulambila kwathu n’kozikidwa pa cidziŵitso colongosoka? (it-1 peji 1260 pala. 2)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Aroma 10:1-15 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Kubwelelako Kaciŵili: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Kubwelelako Kaciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 6)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo a kubwelekako kaciŵili, ndiyeno yambitsani phunzilo poseŵenzetsa buku yakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse. (th phunzilo 9)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuleka Kutsogoza Maphunzilo a Baibo Osapita Patsogolo”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 56
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 36 na Pemphelo