Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 9-11

Fanizo la Mtengo wa Maolivi

Fanizo la Mtengo wa Maolivi

11:16-26

Kodi mbali zosiyana-siyana za mtengo wophiphilitsa wa maolivi ziimila ciani?

  • Mtengo: kukwanilitsidwa kwa colinga ca Mulungu cokhudza cipangano ca Abulahamu

  • Thunthu: Yesu, mbali yaikulu ya mbewu ya Abulahamu

  • Nthambi: a 144,000 amene apanga mbali yaciŵili ya mbewu ya Abulahamu

  • Nthambi ‘zodulidwa’: Ayuda amene anakana Yesu

  • Nthambi ‘zolumikizidwa’: Akhristu odzozedwa na mzimu ocokela m’mitundu yonse

Monga mwa ulosi, mbewu ya Abulahamu, kutanthauza Yesu na a 144,000, adzabweletsa madalitso kwa “anthu a mitundu.”—Aroma 11:12; Gen. 22:18

Niphunzilapo ciani pa mmene Yehova anakwanilitsila colinga cake cokhudza mbewu ya Abulahamu?