Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola luso lathu mu ulaliki—Kuleka kutsogoza maphunzilo a baibo osapita patsogolo

Kunola luso lathu mu ulaliki—Kuleka kutsogoza maphunzilo a baibo osapita patsogolo

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Anthu afunika kuitana pa dzina la Yehova kuti akapulumuke. (Aroma 10:13, 14) Koma sikuti onse amene amavomela kuphunzila Baibo amafuna kutsatila miyezo ya Yehova mu umoyo wawo. Timagwilitsa nchito bwino nthawi yathu ya mtengo wapatali mu ulaliki, mwa kuthandiza anthu amene afunadi kusintha kuti akondweletse Yehova. Ngati wophunzila Baibo sapita patsogolo pambuyo pakuti taphunzila naye kwa nthawi yaitali, cingakhale canzelu kuleka kuphunzila naye, n’colinga cakuti tiseŵenzetse nthawi yathu kuthandiza amene Yehova akuwakokela kwa iye na ku gulu lake. (Yoh. 6:44) Koma ngati munthuyo wasintha, ndipo wakhala na “maganizo abwino” omuthandiza “kukapeza moyo wosatha,” tingayambenso kuphunzila naye Baibo.—Mac. 13:48.

MMENE TINGACITILE:

  • Yamikilani wophunzila wanu cifukwa cofuna kukhala na cidziŵitso colongosoka.—1 Tim. 2:4

  • Gogomezani kufunika koseŵenzetsa zimene waphunzila.—Luka 6:46-49

  • Mwacikondi, kambilanani naye fanizo la Yesu la wofesa mbewu, na kum’pempha kuti aganizile zimene zikumulepheletsa kupita patsogolo.—Mat. 13:18-23

  • Mufotokozeleni mosamala cifukwa cake mudzaleka kuphunzila naye

  • Mudziŵitseni kuti muzimutumila foni mwa apa ndi apo kapena kupitilako kuti muzimulimbikitsa, komanso kuti m’tsogolo mungadzayambenso kuphunzila naye ngati wapanga masinthidwe

TAMBITSANI VIDIYO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi mwaona ciani pa makambilano a mu vidiyo coonetsa kuti wophunzila Baibo sanali kupita patsogolo mwauzimu?

  • Kodi wofalitsa wamuthandiza bwanji wophunzila Baibo kuona kuti afunika kupanga masinthidwe?

  • Kodi wofalitsa waonetsa bwanji kuti ni wokonzeka kudzayambanso kuphunzila naye Baibo?