Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mumawaona Makhalidwe Osaoneka a Mulungu?

Kodi Mumawaona Makhalidwe Osaoneka a Mulungu?

Mukayang’ana duŵa lokongola, nyenyezi, kapena mathithi a madzi, kodi mumaiona nchito ya Mlengi? Cilengedwe cimene timaona cimaonetsa poyela makhalidwe osaoneka a Yehova. (Aroma 1:20) Tikayang’ana zinthu zimene Mulungu analenga, timakwanitsa kuona mphamvu zake, cikondi, nzelu, na cilungamo, komanso kuwolowa manja kwake.—Sal. 104:24.

Ni zinthu zina ziti zimene Yehova analenga zimene mumaona tsiku lililonse? Olo kuti mukhala mu mzinda waukulu, mungathe kuona mitengo na mbalame. Kuyang’anitsitsa cilengedwe ca Yehova kungatithandize kucepetsako nkhaŵa, kuika maganizo athu pa zinthu zofunika, ndiponso kukulitsa cidalilo cakuti Yehova adzatisamalila kwa moyo wathu wonse. (Mat. 6:25-32) Ngati muli ndi ana, athandizeni kuona makhalidwe osaoneka a Yehova. Kuyamikila cilengedwe cimene timaona, kudzatithandiza kumuyandikila kwambili Mlengi wathu.—Sal 8:3, 4.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI ZODABWITSA ZA CILENGEDWE ZIMAONETSA ULEMELELO WA MULUNGU—KUWALA NA MITUNDU, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILA:

  • N’ciani cimatithandiza kuona mitundu ya zinthu?

  • N’ciani cimapangitsa kuti tiziona mitundu yosiyana-siyana pa cinthu cimodzi?

  • N’cifukwa ciani timaona mitundu yosiyana-siyana m’mitambo?

  • Kodi imwe kwanu mumaona mitundu iti yocititsa cidwi m’cilengedwe?

  • N’cifukwa ciani tifunika kuyang’anitsitsa zinthu za m’cilengedwe?

Kodi kuwala na mitundu zimaonetsa ciani cokhudza makhalidwe a Yehova?