UMOYO WATHU WACIKRISTU
Mwai Womanga ndi Wokonza Malo Athu Olambilila
Kuti kacisi wa Yehova amangidwe, panafunikila nchito yaikulu komanso ndalama zambili. Komabe, Aisiraeli anacilikiza nchitoyo mwacangu. (1 Mbiri 29:2-9; 2 Mbiri 6:7, 8) Mmene Aisiraeli anali kusamalila kacisiyo pambuyo pakuti amaliza kumanga, zinali kuonetsa kuti anali kukonda Mulungu kapena ai. (2 Maf. 22:3-6; 2 Mbiri 28:24; 29:3) Masiku ano, Akristu amagwilitsila nchito nthawi yao ndi mphamvu zao pomanga, kuyeletsa, ndi kukonza Nyumba za Ufumu ndiponso Mabwalo a Msonkhano. Kunena zoona, kugwila nchito ndi Yehova mwa njila imeneyi ndi mwai wapadela kwambili, ndipo ndi mbali ya utumiki wathu wopatulika.—Sal. 127:1; Chiv. 7:15.
TINGATHANDIZE PA NCHITOYI MWA . . .
-
Kuyeletsa pambuyo pa misonkhano. Ngati simungathe kutelo, mungatole zinyalala zimene zili pafupi ndi pamene mwakhala.
-
Kugwila nao nchito yoyeletsa ndi kukonza Nyumba ya Ufumu. Pakaculuka ogwila nchito, nchitoyo imasangalatsa ndiponso imapepuka.—lv tsa. 92-93 ndime 18.
-
Kupanga zopeleka za ndalama. Ngakhale titapeleka “timakobidi tiŵili tating’ono,” Yehova amayamikila.—Maliko 12:41-44.
-
Kudzipeleka pa nchito yomanga ndi kukonza nyumba zolambililamo ngati mungathe kutelo. Simufunikila luso lapadela kuti mugwile nao nchito imeneyi.