January 11- 17
2 MBIRI 33–36
Nyimbo 35 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yehova Amaona Munthu Wolapa ndi Mtima Wonse Kukhala Wamtengo Wapatali”: (Mph. 10)
2 Mbiri 33:2-9, 12-16—Manase anakhululukidwa cifukwa analapa zenizeni (w05-CN 12/1 tsa. 21 ndime 5)
2 Mbiri 34:18, 30, 33—Ngati tiŵelenga Mau a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha, akhoza kutikhudza mtima kwambili (w05-CN 12/1 tsa. 21 ndime 10)
2 Mbiri 36:15-17—Sitiyenela kuona cifundo ndi kuleza mtima kwa Yehova mopepuka (w05-CN 12/1 tsa. 21 ndime 7)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu (Mph. 8)
2 Mbiri 33:11—Ndi ulosi uti umene unakwanilitsidwa pamene Manase anatengedwa ku Babulo? (it-1 tsa. 62 ndime 2)
2 Mbiri 34:1-3—Kodi citsanzo ca Yosiya n’colimbikitsa bwanji kwa ife? (w05-CN 12/1 tsa. 21 ndime 6)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kundiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: 2 Mbiri 34:22-33 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa ofalitsa mmene tingagawile magazini a January pogwilitsila nchito nkhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Mlonda, ndi kuyala maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene tingacitele ulendo wobwelelako kwa munthu amene analandila Nsanja ya Mlonda ya January, ndi kuyala maziko a ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene mungacititsile phunzilo la Baibulo. (bh tsa. 9-10 ndime 6-7)
UMOYO WATHU WACIKRISTU
Kulapa n’Kofunika:(Mph. 10) Nkhani yokambidwa ndi mkulu. (w06-CN 11/15 tsa. 27-28 ndime 7-9).
Uzikhululuka ndi Mtima Wonse. (Mph. 5) Nkhani yokambilana. Onetsani vidiyo ya mutu wakuti Uzikhululuka ndi Mtima Wonse. (Pitani pa jw.org, ndi kuona pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANA.) Kenako, pemphani ana kuti akambe zimene aphunzilapo.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia mutu 6 ndime 15-23, bokosi pa tsa. 57, ndi kubwelelamo pa tsa. 58 (Mph. 30)
Bwelezani Mfundo Zimene Taphunzila Komanso Fotokozani Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 6 ndi Pemphelo