January 18- 24
Ezara 1-5
Nyimbo 85 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yehova Amakwanilitsa Malonjezo Ake”: (Mph. 10) [Onetsani Vidiyo Yofotokoza Buku la Ezara.]
Ezara 3:1-6—Maulosi a Yehova amakwanilitsidwa nthawi zonse (w06-CN 1/15 tsa. 19 ndime 2)
Ezara 5:1-7—Yehova angathe kusintha zinthu pofuna kuthandiza anthu ake (w06-CN 1/15 tsa. 19 ndime 4; w86-E 1/15 tsa. 9 ndime 2; w86-E 2/1 tsa. 29 pa kabokosi)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Ezara 1:3-6—N’cifukwa ciani Aisiraeli amene sanasankhe kubwelela ku Yerusalemu sanali ofooka cikhulupililo? (w06-CN 1/15 tsa. 17 ndime 5 ndi tsa. 19 ndime 1)
Ezara 4:1-3—N’cifukwa ciani Ayuda okhulupilika otsalila ku Babulo anakana thandizo? (w06-CN 1/15 tsa. 19 ndime 3)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kundiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: Ezara 3:10–4:7 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Gaŵilani magazini a January pogwilitsila nchito nkhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Galamukani! Ndiyeno yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene tingacitile ulendo wobwelelako kwa munthu amene analandila Galamukani! ya January, ndi kuyala maziko a ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene mungayambitsile phunzilo la Baibulo. (bh tsa. 20-21 ndime 6-8)
UMOYO WATHU WACIKRISTU
“Zina Zonsezi Zidzaonjezedwa kwa Inu”: (Mph. 5) Nkhani yozikidwa pa Mateyu 6:33 ndi Luka 12:22-24. Pemphani ofalitsa kuti afotokoze mwacidule mmene Yehova anakwanilitsila lonjezo lake limeneli mwa kuwapatsa zosoŵa zakuthupi pamene anaika zinthu za Ufumu patsogolo.
Mau Anu Asamakhale—“‘Inde’ Kenako ‘Ai’”?: (Mph. 10) Nkhani Yokambilana yocokela mu Nsanja ya Mlonda ya March 15, 2014, tsamba 30-32.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia mutu 7 ndime 1-14 (Mph. 30)
Kubweleza Mfundo Zimene Taphunzila ndi kufotokoza Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wamaŵa (Mph. 3.)
Nyimbo 41 ndi Pemphelo