EZARA 1–5
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU |Yehova Amakwanilitsa Malonjezo Ake
Yehova analonjeza kubwezeletsa kulambila koona pa kacisi ku Yerusalemu. Koma Aisiraeli atacoka ku ukapolo, anakumuna ndi zopinga zambili, kuonjezela pa lamulo la Mfumu loimitsa kumanga kacisi. Anthu ambili anali kuona monga sadzamaliza kumanga kacisi.
-
c. 537 B.C.E.
Koresi anapeleka lamulo lakuti kacisi afunika kumangidwanso
-
3:3
Mwezi wa 7
Guwa lansembe limangidwa; nsembe zipelekedwa
-
3:10, 11
536 B.C.E.[2a]
Maziko ayalidwa
-
4:23, 24
522 B.C.E.[3a]
Mfumu Aritasasita aimitsa nchito yomanga
-
5:1, 2
520 B.C.E.[3b]
Zekariya ndi Hagai analimbikitsa anthu kuyambilanso nchito yomanga
-
6:15
515 B.C.E.[4]
Kacisi amalizidwa