January 25- 31
Ezara 6–10
Nyimbo 10 ndi Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yehova Amafuna Atumiki Odzipeleka”: (Mph. 10)
Ezara 7:10—Ezara anakonza mtima wake
Ezara 7:12-28—Ezara anakonza zobwelela ku Yerusalemu
Ezara 8:21-23—Ezara anakhulupilila kuti Yehova adzateteza atumiki Ake
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Ezara 9:1, 2—Kodi kukwatilana ndi “anthu a mitundu ina” kunali koopsa motani? (w06-CN 1/15 tsa. 20 ndime 1)
Ezara 10:3—N’cifukwa ciani ana anacotsedwa pamodzi ndi akazi? (w06-CN 1/15 tsa. 20 ndime 2)
Kodi kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kundiphunzitsa ciani za Yehova?
Ndi mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingagwilitsile nchito mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: Ezara 7:18-28 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
KUONJEZELA LUSO LANU MU ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene tingagaŵile kabuku ka Uthenga Wabwino. Acitsanzo akambilane phunzilo 8, funso 1, ndime 1, ndi kuyala maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene tingacitile ulendo wobwelelako kwa munthu amene analandila kabuku ka Uthenga Wabwino. Akambilane phunzilo 8, funso 1, ndime 2 ndi kuyala maziko a ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) Citani citsanzo coonetsa mmene mungacititsile phunzilo la Baibulo pogwilitsila nchito phunzilo 8, funso 2, m’kabuku ka Uthenga wabwino.
UMOYO WATHU WACIKRISTU
“Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyala Maziko a Ulendo Wobwelelako”: (Mph. 7) Nkhani yokambilana. Onetsani vidiyo Yophunzitsa Maluso a mu Ulaliki ya mwezi wa January imene ionetsa zimene wofalitsa ayenela kucita poyala maziko a ulendo wobwelelako atagaŵila Nsanja ya Mlonda ya January-February, Galamukani! ya January, ndi kabuku ka Uthenga Wabwino.
Zosoŵa za Pampingo: (Mph. 8)
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: ia mutu 7 ndime 15-27, ndi kubwelelamo pa tsa. 66 (Mph. 30)
Bwelezani Mfundo Zimene Taphunzila Komanso Fotokozani Zomwe Tidzaphunzila Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 120 ndi Pemphelo