Maulaliki Acitsanzo
NSANJA YA MLONDA
Funso: Anthu ambili amaona kuti Baibulo ndi buku lofunika kwambili, koma amaganiza kuti n’zosatheka kulimvetsetsa. Kodi inu mumaliona bwanji Baibulo?
Lemba: Aroma 15:4
Kugaŵila cofalitsa: Magazini iyi ikufotokoza umboni woonetsa kuti n’zotheka kumvetsetsa Baibulo. Ikufotokozanso zimene zingatithandize kulimvetsetsa.
GALAMUKANI!
Kugaŵila cofalitsa: Ndakubweletselani Galamukani! ya mwezi uno.
Funso: Taonani funso ili patsamba 2 komanso zimene anthu ambili amayankha. Nanga inu muganiza bwanji?
Lemba: Miy. 24:10 Nkhani iyi ifotokoza mfundo zina zothandiza.
UTHENGA WABWINO WOCOKELA KWA MULUNGU
Kugaŵila cofalitsa: Ndabwela kudzakuuzani za phunzilo laulele la Baibulo. Kabuku aka kangakuthandizeni kudziŵa pamene mungapeze mayankho a mafunso ofunika kwambili m’Baibulo lanu.
Funso: Kodi munaphunzilapo Baibulo? [Yembekezani yankho.] Lekani ndikuonetseni mmene timaphunzilila. [Kambilanani funso 1 m’phunzilo 2.]
Lemba: Chiv. 4:11
LEMBANI ULALIKI WANU
Onani maulaliki acitsanzo amene asonyezedwa kale kuti akuthandizeni kulemba ulaliki wanu.