January 16-22
YESAYA 34-37
Nyimbo 31 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Hezekiya Anafupidwa Cifukwa ca Cikhulupililo Cake”: (10 min.)
Yes. 36:1, 4-10, 15, 18-20—Asuri anatonza Yehova ndi kuopseza anthu ake (ip-1 peji 386-388 pala. 7-14)
Yes. 37:1, 2, 14-20—Hezekiya anadalila Yehova (ip-1 peji 389-391 pala. 15-17)
Yes. 37:33-38—Yehova anacitapo kanthu kuteteza anthu ake (ip-1 peji 391-394 pala. 18-22)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min. )
Yes. 35:8—Kodi “Mseu wa Ciyelo” unali ciani? Ndipo n’ndani anali woyenelela kuyendamo? (w08 5/15 peji 26 pala. 4; peji 27 pala. 1)
Yes. 36:2, 3, 22—Kodi Sebina anaonetsa bwanji citsanzo cabwino ca kulandila uphungu? (w07 1/15 peji 8 pala. 6)
Kodi ine pacanga, kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno zimene ine pacanga ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. kapena zocepelapo) Yes. 36:1-12
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. kapena zocepelapo) Mat. 24:3, 7, 14—Phunzitsani Coonadi—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 min. kapena zocepelapo) 2 Tim. 3:1-5—Phunzitsani Coonadi—Musiileni khadi ya JW. ORG.
Phunzilo la Baibo: (6 min. kapena zocepelapo) bh peji 31-32 pala. 11-12—Itanilani munthuyo ku misonkhano.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Nyimbo na 91
“Inu Mulungu Wanga, Cikhulupililo Canga Cili mwa Inu”: (15 min.) Mafunso na mayankho. Yambani mwa kutambitsa kambali ka vidiyo yakuti “Inu Mulungu Wanga, Cikhulupililo Canga Cili mwa Inu” (Yendani ku mavidiyo pa MISONKHANO NA UTUMIKI WATHU).
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 7 pala. 1-9
Kubwelelamo na Kuchulako za Mlungu Wotsatila (3 min.)
Nyimbo 96 na Pemphelo