January 2- 8
YESAYA 24-28
Nyimbo 12 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yehova Amasamalila Anthu Ake”: (10 min.)
Yes. 25:4, 5—Yehova amateteza onse amene amam’tumikila (ip-1 272 pala. 5)
Yes. 25:6—Yehova wakwanilitsa lonjezo lake la kupeleka cakudya cauzimu ca mwana alilenji (w16.05 24 pala. 4; ip-1 273 mapa. 6-7)
Yes. 25:7, 8—Posacedwa, ucimo na imfa zidzacotsedwa kothelatu (w14 9/15 26 pala. 15; ip-1 273-274 pala. 8-9)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yes. 26:15—Kodi tingathandizile bwanji pamene Yehova ‘afutukulila kutali malile onse a dziko’? (w15 7/15 11 pala. 18)
Yes. 26:20—N’ciani cikuyelekezedwa na ‘zipinda za mkati’? (w13 3/15 23 pala. 15-16)
Kodi ine pacanga, kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno zimene ine pacanga ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. kapena zocepelapo) Yes. 28:1-13
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (15 min.) Kukambilana “Maulaliki a Citsanzo.” Tambitsani vidiyo ya citsanzo iliyonse ndi kukambilana zimene mwaphunzilapo. Pambuyo potamba vidiyo yoonetsa mmene tingagaŵile kabuku ka Uthenga, kambilanani nkhani yakuti, Mmene Tingatsogozele Phunzilo m’Kabuku ka Uthenga Wabwino, yopezaka m’kabuku ka Umoyo na Utumiki ka January 2016, papeji 8.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Zosoŵa za Pampingo: (15 min.) Mungasankhe kukambilana zimene tiphunzilapo m’nkhani yopezeka m’Buku Lapacaka la 2016 peji 140-142
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 6 pala. 8-15, na bokosi papeji 63
Kubwelelamo na Kuchulako za Mlungu Wotsatila (3 min.)
Nyimbo 66 na Pemphelo