Maulaliki a citsanzo
NSANJA YA MLONDA
Funso: Anthu ena amaganiza kuti Baibo inasila nchito, koma ena amakhulupilila kuti ikali yothandiza maningi. Nanga imwe muganiza bwanji?
Lemba: 2 Tim. 3:16, 17
Cogaŵila: Nsanja ya Mlonda iyi ifotokoza malangizo othandiza opezeka m’Baibo. Ndipo ionetsa zimene mungacite kuti mupindule na zimene mumaŵelenga m’Baibo.
PHUNZITSANI COONADI
Funso: Kodi mapeto a dziko ali pafupi?
Lemba: Mat. 24:3, 7, 14
Mfundo ya Coonadi: Maulosi a m’Baibo aonetsa kuti tili m’masiku otsiliza. Koma umenewu ni uthenga wabwino—cifukwa ni umboni wakuti zinthu zabwino zili pafupi.
UTHENGA WABWINO WOCOKELA KWA MULUNGU
Cogaŵila: Nabwela kudzakuuzani za phunzilo laulele la Baibo. Kabuku aka kangakuthandizeni kudziŵa pamene mungapeze mayankho pa mafunso ofunika kwambili m’Baibo yanu?
Funso: Kodi munaphunzilapo Baibo? Lekani nikuonetseni mmene timaphunzilila. [Kambilanani funso 1, m’phunzilo 2]
Lemba: Chiv. 4:11
KONZANI ULALIKI WANU
Funso:
Lemba:
Cogaŵila: