UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO January 2018
Makambilano a Citsanzo
Zitsanzo za makambilano otsatizana okamba za kufunika kwa Baibo masiku ano.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Ufumu Wakumwamba Wayandikila”
Yohane anali na umoyo wosalila zambili, wodzipeleka pa kucita cifunilo ca Mulungu. Masiku ano, kukhala na umoyo wosalila zambili kudzatithandiza kucita zambili potumikila Mulungu.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Zimene Tiphunzilapo pa Ulaliki wa Yesu wa Paphili
Kodi kuzindikila zosoŵa zathu zauzimu kumatanthauza ciani? Nanga tingawonjezele bwanji zimene timaphunzila pa pulogilamu yathu yauzimu?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pita Ukayanjane ndi M’bale Wako Coyamba—Motani?
Kodi Yesu anaphunzitsa kuti pali mgwilizano wanji pakati pa kukhala mwamtendele na m’bale wathu na kulambila Mulungu movomelezeka?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Pitilizani Kufuna-funa Ufumu Coyamba
Pa zinthu zonse zimene tingapemphelele, ni cinthu citi cimene tifunika kuciika patsogolo?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Lekani Kuda Nkhawa
Pa Ulaliki wake wa pa Phili, kodi Yesu anatanthauza ciani pamene anauza ophunzila ake kuti aleke kuda nkhawa?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Yesu Anali Kukonda Anthu
Pamene Yesu anacilitsa anthu, anaonetsa mphamvu zake, koma koposa zonse anaonetsa cikondi cake na cifundo cake kwa anthu.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Yesu Anali Kutsitsimula Anthu
Pamene tinasenza goli lokhala wophunzila wa Yesu pa ubatizo wathu, timagwila nchito yovuta na kulandila maudindo. Ngakhale n’conco, kucita zimenezi n’kotsitsimula.