January 1-7
MATEYU 1-3
Nyimbo 14 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Ufumu Wakumwamba Wayandikila”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Mateyu.]
Mat. 3:1, 2—Yohane M’batizi anali kulengeza kuti Mfumu ya m’tsogolo ya Ufumu wa kumwamba idzaonekela posacedwa (“Kulalikila,” “Ufumu,” “Ufumu wakumwamba,” “wayandikila” pa Mat. 3:1, 2 nwtsty mfundo zounikila)
Mat. 3:4—Yohane M’batizi anali na umoyo wosalila zambili, ndipo anali wodzipeleka kothelatu pocita cifunilo ca Mulungu. (“Covala ca Yohane M’batizi na Kaonekedwe Kake,” “Dzombe,” “Uci” zithunzi pa Mat. 3:4 nwtsty)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Mat. 1:3—M’buku la Mateyu, n’cifukwa ciani pa mzela wobadwila wa Yesu, wa amuna okha-okha, anaphatikizaponso azimayi asanu? (“Tamara” mfundo younikila pa Mat. 1:3 nwtsty)
Mat. 3:11—Tidziŵa bwanji kuti munthu pobatizika afunika kumila thupi lonse m’madzi? (“ndidzakubatizani” mfundo younikila pa Mat. 3:11 nwtsty)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Mat. 1:1-17
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyo.
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (3 min. olo kucepelelapo) Onani Makambilano a Citsanzo.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) bhs mape. 41-42 mapa. 6-7
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Lipoti la Caka Cautumiki: (15 min.) Nkhani ya mkulu. Mukaŵelenga kalata yocokela ku ofesi ya nthambi yokamba za lipoti la caka cautumiki, funsani mafunso ofalitsa amene munawasankhilatu, amene anakhala na zocitika zabwino mu utumiki caka catha.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy Mutu 2
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 137 na Pemphelo