January 22-28
MATEYU 8-9
Nyimbo 17 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yesu Anali Kukonda Anthu”: (10 min.)
Mat. 8:1-3—Yesu anaonetsa cifundo cacikulu kwa munthu wakhate (“n’kumukhudza,” “Ndikufuna” mfundo zounikila younikila pa Mat. 8:3,nwtsty)
Mat. 9:9-13—Yesu anali kukonda anthu ozondewa na ena (“kudya patebulo,” “okhometsa msonkho” mfundo zounikila pa Mat. 9:10, nwtsty)
Mat. 9:35-38—Kukonda anthu kunalimbikitsa Yesu kulalikila uthenga wabwino ngakhale pamene anali wolema. Analinso kupempha Mulungu kuti atumize anchito ambili (“anawamvela cisoni” mfundo younikila pa Mat. 9:36, nwtsty)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Mat. 8:8-10—Tingaphunzilepo ciani pa zimene Yesu anakambilana na kapitawo wa asilikali? (w02 8/15 peji 13 pala. 16)
Mat. 9:16, 17—Kodi Yesu anafuna kumveketsa mfundo yanji pa mafanizo aŵiliwa? (jy peji 70 pala. 6)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Mat. 8:1-17
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Wobwelelako Waciŵili: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano a citsanzo. Itanilani munthuyo ku misonkhano.
Ulendo Wobwelelako Wacitatu: (3 min. olo kucepelapo) Sankhani mwekha lemba na kugaŵila cofalitsa cophunzitsila Baibo.
Phunzilo la Baibo: (6 min. olo kucepelapo) bhs mape. 46-47 mapa. 18-19
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
‘Ndithu Mulungu Anamuika Kukhala Ambuye ndi Khristu’—Mbali 1, Kambali kake: (15 min.) Kukambilana. Mukaŵelenga Mateyu 9:18-25 na kutamba kavidiyo, kambilanani mafunso aya:
Kodi Yesu anacita ciani coonetsa kuti anaganizila mkazi wodwala ndiponso Yairo?
Kodi nkhani imeneyi imakhudza bwanji mmene mumaonela maulosi a m’Baibo okamba zimene Ufumu udzacita?
Tingaonetse m’njila ziti kuti timakonda anthu mmene Yesu anali kuwakondela?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 5
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 95 na Pemphelo