UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pita Ukayanjane ndi M’bale Wako Coyamba—Motani?
Yelekezelani kuti mukhala mu mzinda wa Galileya, ni m’nthawi ya Yesu. Ndiye mwapita ku Yerusalemu kukacita Cikondwelelo ca Misasa. Kumeneko, olambila anzanu ocokela kutali ali pilingu-pilingu. Lomba mufuna kupeleka nsembe kwa Yehova. Conco, mwatenga mbuzi na kuuyamba ulendo wopita ku kacisi, ndipo mudutsa m’cigulu ca anthu ambili. Mutafika pakacisi, mupeza kuti pali anthu ambili ofunanso kupeleka nsembe. Kenako, cafika pa imwe kuti mupeleke mbuzi yanu kwa ansembe. Koma mukumbukila kuti m’bale wanu, amene mwina ali m’cigulu ca anthu pakacisipo, kapena kwinakwake mumzindawo, ali namwe cifukwa. Ndiyeno Yesu akuuzani zimene mufunika kucita. (Ŵelengani Mateyu 5:24) Kodi imwe na m’bale wanu amene anakulakwilani mungacite ciani kuti mubwezeletse mtendele potsatila malangizo a Yesu? Pa mndandanda uliwonse uli pansipa, congani yankho loyenelela.
MUYENELA . . .
-
kukamba na m’bale wanu pokhapo ngati mwaona kuti alidi na cifukwa comveka cokhumudwila
-
kuyesa kuwongolela maganizo a m’bale wanu ngati muona kuti ali cabe na mtima wapacala, kapena kuti nayenso analengetsa vutolo
-
kumvetsela modekha pamene m’bale wanu akufotokoza mmene akumvelela. Ndipo ngakhale ngati simunakhutile kweni-kweni na zimene wakamba, m’pepeseni pa kukhumudwa kwake, kapena pa zimene munacita
M’BALE WANU AYENELA . . .
-
kufuna-funa amene angamucilikize mu mpingo mwa kuwauza zimene munamulakwila
-
kukukalipilani, kukamba zonse zimene munamulakwila, na kufuna kuti mpaka muvomeleze colakwa canu
-
kuganizila kudzicepetsa kwanu na kulimba mtima kwanu pomufikila, ndipo akukhululukileni na mtima wonse
Olo kuti masiku ano sitipeleka nsembe za nyama polambila, kodi Yesu anaphunzitsa kuti pali mgwilizano wanji pakati pa kukhala mwamtendele na m’bale wathu na kulambila Mulungu movomelezeka?