UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Sankhani Kutumikila Yehova
Ngati ndimwe Mkhristu wacinyamata wosabatizika kapena wophunzila Baibo, kodi muli na colinga cokabatizika? N’cifukwa ciani muyenela kubatizika? Kudzipatulila na kubatizika kudzakuthandizani kukhala pa ubale wapadela na Yehova. (Sal. 91:1) Kudzakuthandizaninso kuti mukapulumuke. (1 Pet. 3:21) N’ciani cingakuthandizeni kuti mufike pa kudzipatulila na kubatizika?
Muyenela kukhutila inu mwini kuti zimene muphunzila ni coonadi. Mukakhala na mafunso, fufuzani. (Aroma 12:2) Dziŵani mbali zimene mungafunike kuwongolela, ndipo sinthani n’colinga cakuti mukondweletse Yehova. (Miy. 27:11; Aef. 4:23, 24) Nthawi zonse muzipemphela kwa iye kuti akuthandizeni. Khalani otsimikiza kuti Yehova adzakulimbitsani na kukucilikizani na mphamvu yake ya mzimu woyela. (1 Pet. 5:10, 11) Mukayesetsa mwakhama mudzapindula. Kutumikila Yehova ndiko kofunika kwambili pa umoyo!—Sal. 16:11.
ONETSANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE MUNGACITE KUTI MUYENELELE UBATIZO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
Kodi ena agonjetsa zopinga zanji kuti ayenelele ubatizo?
-
Mungacite ciani kuti mukhale na cikhulupililo cofunikila kuti mudzipatulile kwa Yehova?
-
N’ciani casonkhezela ena kupanga masinthidwe ofunikila kuti ayenelele ubatizo?
-
Kodi Yehova amawadalitsa bwanji anthu amene amasankha kum’tumikila?
-
Kodi kudzipatulila na kubatizika kutanthauza ciani?