February 22-28
NUMERI 5–6
Nyimbo 81 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Mungatengele Bwanji Citsanzo ca Anazili?”: (Mph. 10.)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu (Mph. 10.)
Num. 6:6, 7—Kodi zinatheka bwanji kuti Samisoni agwile mitembo ya anthu amene anafa koma n’kupitilizabe kukhala Mnazili? (w05 1/15 30 ¶2)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4.) Num. 5:1-18 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3.) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno chulani na kukambilana vidiyo yakuti Mboni za Yehova—Kodi Ndife Anthu Otani? (koma musaitambitse) (th phunzilo 1)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4.) Yambani na makambilano acitsanzo. Gaŵilani cofalitsa ca mu Thuboksi yathu. (th phunzilo 3)
Nkhani: (Mph. 5.) w06 1/15 32—Mutu: Zinthu Zocititsa Cidwi Zimene Anapeza Zoonetsa Kuti Baibo Ni Yolondola Pofotokoza Mbili Yakale. (th phunzilo 13)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kodi Mudzacitako Upainiya Wothandiza m’Mwenzi wa March Kapena April?”: (Mph. 5.) Kukambilana.
Kampeni Yomemeza Anthu ku Cikumbutso Idzayamba pa Ciŵelu, February 27: (Mph. 10.) Kukambilana. Gaŵilani aliyense m’gulu kapepa koitanila anthu ku Cikumbutso, na kukambilana mwacidule zimene zilimo. Fotokozani makonzedwe a pampingo panu a mokafolela magawo. Tambitsani vidiyo ya ulaliki wacitsanzo. Ndiyeno funsani omvetsela mafunso awa: Ni pa nthawi iti pamene tiyenela kutambitsa vidiyo yakuti Kukumbukila Imfa ya Yesu? Kodi mwininyumba angaonetse cidwi m’njila zina ziti?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30.) lfb phunzilo 23, 24
Mawu Othela (Mph. 3.)
Nyimbo 49 na Pemphelo