Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Misonkhano Ikulu-ikulu Yapacaka Imatipatsa Mwayi Woonetsana Cikondi

Misonkhano Ikulu-ikulu Yapacaka Imatipatsa Mwayi Woonetsana Cikondi

N’cifukwa ciani misonkhano yathu ikulu-ikulu yapacaka imatisangalatsa kwambili? Monga mmene zinalili m’nthawi ya Aisiraeli, misonkhano ikulu-ikulu masiku ano imatipatsa mwayi wolambila Yehova pamodzi na okhulupilila anzathu mahandiledi, ngakhale masauzande kumene. Timakondwela na phwando la cakudya cauzimu conona. Timasangalalanso na mwayi wamtengo wapatali woyanjana na mabwenzi komanso mabanja athu. Timayamikila kwambili misonkhano imeneyi, cakuti timayesetsa kupezekapo masiku onse atatu.

Tikakhala na mwayi wosonkhana pamodzi, sitiyenela kungoganizila za mmene ife tingapindulile, koma tiyenela kuganizilanso za mmene tingaonetsele cikondi kwa ena. (Agal. 6:10; Aheb. 10:24, 25) Ngati titsegulila m’bale kapena mlongo wathu citseko kapena kusungila malo anthu okhawo amene tili nawo limodzi, timaonetsa kuti timaganizila zofuna za ena. (Afil. 2:3, 4) Misonkhano ikulu-ikulu imatipatsa mwayi wopanga mabwenzi atsopano. Pulogilamu isanayambe kapena ikatha, komanso pa nthawi yopumula, tingakhale na colinga codziŵana na winawake amene sitim’dziŵa. (2 Akor. 6:13) Ubwenzi umene tingapange pa zocitika zaconco, ungakhale mpaka kale-kale. Koposa zonse, anthu ena akaona cikondi ceni-ceni cimene timaonetsana, angasankhe kuyamba kutumikila nafe Yehova pamodzi.—Yoh. 13:35.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI MSONKHANO WA MAIKO WAKUTI “CIKONDI SICITHA”! NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi abale na alongo ocokela ku maiko ena anaonetsedwa bwanji cikondi pa misonkhano ya maiko ya mu 2019?

  • N’cifukwa ciani mgwilizano na cikondi zimene zili pakati pa anthu a Yehova n’zocititsa cidwi?

  • Kodi abale a m’Bungwe Lolamulila anafotokoza mbali ziti za cikondi cacikhristu?

  • Kodi mungacite ciani kuti muthandizile kuonetsa cikondi pa misonkhano yathu ikulu-ikulu?

    Kodi cikondi cacikhristu cinawagwilizanitsa bwanji abale athu ku Germany na ku South Korea?

  • Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciani?