CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Caka ca Ufulu Komanso Ufulu Wam’tsogolo
Caka ca ufulu cinali kuthandiza Aisiraeli kuti asakhale na nkhongole yosatha komanso umphawi wosatha (Lev. 25:10; it-1 871; onani cithunzi pacikuto)
Kugulitsa malo kunali monga kucititsa lendi cabe, ndipo mtengo wake unali kutengela pa phindu limene wogulayo adzapeza pa zokolola za pa malopo (Lev. 25:15; it-1 1200 ¶2)
Yehova anali kuwadalitsa anthu ake akamvela lamulo lokhudza Caka ca Ufulu (Lev. 25:18-22; it-2 122-123)
Posacedwa, anthu okhulupilika adzasangalala mokwanila na madalitso m’Caka ca Ufulu cophiphilitsila pamene adzamasulidwa kothelatu ku ucimo na imfa.—Aroma 8:21.
Kodi aliyense wa ife ayenela kucita ciani kuti akapeze ufulu umene Yehova anatilonjeza?