UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Makolo, Phunzitsani Ana Anu Zimene Afunika Kudziŵa
Tikhala m’dziko limene limafuna kuti tiziona monga cabwino ni coipa ndipo coipa ni cabwino. (Yes. 5:20) N’zacisoni kuti anthu ena m’dzikoli, amacita zinthu zimene Yehova amadana nazo kuphatikizapo kucita zinthu zosayenela pakati pa amuna okha-okha kapena akazi okha-okha. Ana athu ni amtengo wapatali. Koma anzawo kusukulu ndi anthu ena angayese kuwanyengelela kuti azitsatila zocita zawo. Kodi mungawakonzekeletse bwanji ana anu ku mayeselo amenewa na ena otelo?
Konzekeletsani ana anu mwa kuwaphunzitsa mfundo za Yehova. (Lev. 18:3) Malinga na msinkhu wawo, pang’ono-m’pang’ono aphunzitseni zimene Baibo imakamba pa nkhani ya kugonana. (Deut. 6:7) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ana anga n’nawaphunzitsa za kuonetsana cikondi m’njila yoyenela, kufunika kovala mwaulemu, komanso kufunika kwakuti ena azipewa kuwagwila kumalo obisika kapena kuwaonela? Kodi ana anga adziŵa zoyenela kucita ngati wina afuna kuwaonetsa zithunzi zamalisece, kapena ngati wawapempha kuti acite zinthu zimene Yehova amati n’zoipa?’ Kudziŵilatu zocita kungawathandize kupewa kugwela m’mavuto. (Miy. 27:12; Mlal. 7:12) Ngati muphunzitsa ana anu, mumaonetsa kuti mumakonda coloŵa canu camtengo wapatali cocokela kwa Yehova.—Sal. 127:3.
ONETSANI VIDIYO YAKUTI MANGANI NYUMBA IMENE IDZAKHALITSA—TETEZANI ANA ANU KU “ZINTHU ZOIPA,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
N’cifukwa ciani makolo ena amaopa kuunikila ana awo pankhani zakugonana?
-
N’cifukwa ciani makolo ayenela kulela ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake”?—Aef. 6:4
-
Kodi gulu la Yehova lapeleka zida zotani zothandiza makolo kuunikila ana awo pankhani zakugonana?—w19.05 12, bokosi
-
N’cifukwa ciani mufunika kumakambilana kaŵili-kaŵili na ana anu pasanabuke mavuto aakulu?