February 28–March 6
1 SAMUELI 9-11
Nyimbo 121 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Poyamba Sauli Anali Wodzicepetsa”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
1 Sam. 9:9—Kodi n’kutheka kuti mawu amenewa anali kutanthauza ciani? (w05 3/15 22 ¶8)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 1 Sam. 9:1-10 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
“Wonjezelani Cimwemwe Canu mu Ulaliki—Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kupewa Mayanjano Oipa”: (Mph. 10) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Thandizani Maphunzilo Anu a Baibo Kupewa Mayanjano Oipa.
Nkhani: (Mph. 5) w15 4/15 6-7 ¶16-20—Mutu: Zimene Zingakuthandizeni Kuphunzitsa Bwino Ena. (th phunzilo 19)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Lipoti la Caka ca Utumiki: (Mph. 15) Nkhani yokambidwa na mkulu. Pambuyo poŵelenga cilengezo cocokela ku ofesi ya nthambi cokhudza lipoti la caka ca utumiki, funsani mafunso ofalitsa amene munawakonzekeletsa pasadakhale kuti asimbe zokumana nazo zolimbikitsa za mu ulaliki m’caka capita ca utumiki.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 79
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 17 na Pemphelo