February 20-26
1 MBIRI 17-19
Nyimbo 110 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Khalanibe Acimwemwe Ngakhale Pamene Mwakumana na Zolefula”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
1 Mbiri 17:16-18—Mofanana na Davide, kodi tingakhale otsimikiza za ciyani? (w20.02 12, bokosi)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulila iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 1 Mbiri 18:1-17 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. Chulani na kukambilanako vidiyo yakuti Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? (Koma musaitambitse.) (th phunzilo 17)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. M’gaŵileni cofalitsa ca m’Thuboksi yathu. (th phunzilo 3)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lff phunzilo 09 mfundo 4 (th phunzilo 9)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Lipoti la Caka ca Utumiki: (Mph. 15) Kukambilana. Ŵelengani cilengezo ca ku ofesi ya nthambi cokhudza lipoti la caka ca utumiki. Kenako, pemphani gulu kuti lifotokoze zocitika zosangalatsa za mu Lipoti la Caka ca Utumiki ca 2022 la Mboni za Yehova Padziko Lonse. Funsani mafunso ofalitsa amene munawakonzekeletsa kuti asimbe zocitika zolimbikitsa za mu ulaliki m’caka capita ca utumiki.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 38 mfundo 1-4
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 141 na Pemphelo