Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Dziikileni Zolinga za pa Nyengo ya Cikumbutso

Dziikileni Zolinga za pa Nyengo ya Cikumbutso

Caka ciliconse, ife anthu a Yehova timayembekezela mwacidwi kusonkhana pamodzi kuti ticite Cikumbutso. Kwa milungu ingapo Cikumbutso cisanacitike komanso pambuyo pake, timaseŵenzetsa mipata yapadela imene timakhala nayo kuti titamande Yehova na kumuyamikila cifukwa ca mphatso ya dipo. (Aef. 1:3, 7) Mwacitsanzo, timayesetsa mmene tingathele kuitanila ena ku Cikumbutso. Ena amakwanitsa kusinthako zinthu zina pa umoyo wawo kuti aciteko upainiya wa maola 30 kapena 50 m’mwezi wa March kapena April. Kodi mungakonde kuwonjezela nthawi imene mumathela mu ulaliki pa nyengo ya Cikumbutso imene ikubwelayi? N’ciyani cingakuthandizeni kucita zimenezi?

Timacita zambili tikakonzekela pasadakhale. (Miy. 21:5) Popeza nyengo ya Cikumbutso ili pafupi, ino ndiyo nthawi yoyamba kukonzekela. Ganizilani mmene mungawonjezele utumiki wanu pa nyengo ya Cikumbutso, komanso zimene muyenela kucita kuti mukwanilitse zolinga zanu. Ndiyeno pemphani Yehova kuti adalitse zoyesayesa zanu.—1 Yoh. 5:14, 15.

Ni njila zina ziti zimene mungawonjezele utumiki wanu pa nyengo ya Cikumbutso?